The Minister's Speech | [Read Speech in English]

Speech by Hon. Kamangadazi Chambalo, Minister of Youth, Sports and Culture (Monday, April 7, 1997, Blantyre)

  1. Mkulu wa malo ano
  2. Inu bambo Mwangwego
  3. Akuluakulu a Boma amene ndachokera nawo ku Unduna
  4. Amayi ndi abambo

Ena ake akulankhula kudzanena kuti ifeyo a Malawi takhala tikukopera zinthu zaeni kwa nthawi yayitali. Chimodzi mwa chimene takoperacho ndi chizungu chimene ndimabvutika nacho pano. Ndimakhumbira anzanga awa, akungolankhula osayang’ananso pa pepala iyayi. Ndiye ndikukhulupilira kuti mawa ndi mkucha lino, nafenso, ngakhale ku Nyumba Yamalamulo mudzatilola a Malawi kuti tizilankhula mchichewa eti?
Koma kubwerera nkhani iyi ya mtunda uwu wa a Mwangwego, nkhani imeneyi ine ndili nayo chidwi kwambiri. Ngakhale kuti munthu sutonza muunda wa makolo ako, koma ine ndikuti zimenezi si akanachita makolo athu kalekale? Nafenso tikamapita ku Ethiopia, ku Somalia, kaya ku Sri Lanka, ku India nkumakanyadiranso kuti makolo athu anachita izi. Komabe, sitinachedwe kwenikweni iyayi. Chauta watipatsa anthu kudzera mwa a bambo Mwangwego.
Ndikhulupila kuti zimene akupanga bambo Mwangwego, tonsefe a Malawi, boma, makampani ndi onse muno mu Malawi, tiathandize a Mwangwego kuti malemba amenewa akhale ndithu akuya kuti zilankhulidwe zathu tizilemba ndi malemba amenewa.
Munadzalalankhula nkhani ya chithandizo chochokera ku boma. Boma likapanda kuthandiza apa, ndidabwatu.
Pomaliza, ndipemphe kuti kope yija yachepa. Mundipatse kope yina kuti ndikapatse bwana prezidenti kuti ndikamakafotokoza, ndizikafotokoza ndi kena kake m’manja.
Ineyo pandekha, komanso ngati nduna ya zachikhalidwe chathu, komanso m’malo mwa boma ndili wonyadira kwambiri ndipo ndikufunireni zonse zabwino a Mwangwego ndi gulu lanu lonse kuti ntchito yimeneyi yipitilire.

Zikomo kwambiri.

 
Copyright 2011 Mwangwego. All Rights Reserved. Design By Patkay Graphics.
Access Webmail